Dr. Triephornia Mpinganjira adyetsa anthu mgonelo mwa ulele
Dr. Triephornia Thomson Mpinganjira, yemwe ndi mkazi wa mpondamatiki Dr. Thomson Mpinganira, wati anthu akadya chakudya cha madzulo ku Bingu International Convention centre (BICC) mu mzinda wa Lilongwe lero pa “bill” yake.
Dr. Triephornia, omwenso ndi dziwika bwino pa nkhani za malonda m’dziko muno ngakhalenso mayiko akunja, ati iyi ndi njira imodzi yowathokozera anthu amene amamutsata pa tsamba lake la mchezo pa Facebook.
Malingana ndi zomwe alemba pa tsamba lawo la mchezo, Mai Mpinganjira ati iwo akuthokoza anthu-wa kaamba ka kudekha pa nthawi imene tsamba lawo linabedwa ndi anthu a chipongwe ndipo ati tsambali tsopano lidabwezeretsedwa.
Mai Mpinganjira ati anthu amene ali omutsatila kwambiri (top fans pachingerezi) ochokera mu mzinda wa Lilongwe ndi amene akuyitanidwa kuyambila nthawi ya 5:30 madzulo a lero ndipo malo odyera atsekedwa 6:15.
Mayi Dr. Triephornia Thomson Mpinganjira amadziwikanso bwino ndi kuthandiza anthu ovutika m’dziko muno.
The post Dr. Triephornia Mpinganjira adyetsa anthu mgonelo mwa ulele appeared first on Malawi Voice.